Maphunziro a adindo oona za ana m’boma la Chikhwawa

Ife a Law Commission tinapitanso mmudzi mwa a Gulupu Chizenga kwa mfumu yaikulu Ngabu ku Chikwawa kumene timaphunzitsa adindo osiyanasiyana za malamulo oteteza ana ku nkhanza.
Cholinga cha maphunzirowa chinali chodziwitsa adindo monga mafumu komanso atetezi a ana malamulo okhudza ana komanso mmene angatetezere ana ku nkhanza kumanso kudziwitsa ena za malamulowa m’dera mwawo.
Kumamaliziro a maphunzirowa lero, adindowa anali ndi mwambo wofotokozera anthu a dera lina za malamulowa.
Maphunzirowa anakonzedwa ndi bungwe la NGO Coalition on Child Rights mogwirizana ndi Unduna Owona kuti Pasakhale Kusiyana pakati pa Amayi ndi Abambo, ana ndi chisamaliro cha anthu.
Iyi ndi imodzi mwa ndondomeko zimene bungwe la Law Commission imapanga pogwirana manja ndi mabungwe ena kufikira anthu mmidzi ndi kuphunzitsa malamulo a dziko lino la Malawi.

Similar Posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *